Our way of lifeChinyanja proverb

Makhalidwe Athu

Perekani Nthano
`

Makhalidwe Athu

Nchito ya Makhalidwe Athu Ana Onse Kuwerenga (All Children Reading Project - ACR) ili ndi cholinga chopititsa patsogolo luso ya kuwerenga m’magiledi achiyambi pakupereka zowerenga zapadela komanso uthandiza aphunzi kuwerenga upyolera pa malamya am’manja. Nchito ya miyezi khumi, asanu ndi itatuyi ili ndi zolinga izi:
1) udzetsa nkupititsa patsogolo chilakolako chakuwerenga kunyumba pakati pa aphunzi.
2) uchulukitsa nthawi imene aphunzi awerenga kunyumba.
3) uchulukitsa nthawi imene banja ithandizila mphunzi kuwerenga pomwe ali kunyumba.

0+
Aphunzi
0+
Nthano
0+
Kupereka

M’mene tikuchitira

Nsanja

SMS

Mauthenga afupi afupi - Short Message Service (SMS) agwiritsidwa nchito utumiza nthano sabata iliyonse ku makolo a aphunzi mzigawo zitatu, pa Lolemba, Chitatu ndi pa Chisanu. Chigawo chilichonse cha nthano chili ndi funso lofunika kuyankhidwa. Anthu nawonso angatumize nthano zawo upyolera mu uthenga wa pa lamya wa SMS pakuyambira kulemba mau akuti “Nthano”, omwe ali ngati mfungulo, kenaka upitiliza ndi uthenga wa nthano.

IVR

Makolo ndi anthu onse angatengeko mbali potuma lamya ku luso yakumvetsera pa lamya yochedwa Interactive voice response (IVR) imene ngati aitumila, mwaiyo yokha idzaduka kenana iyo kuwatumila, kuwalola kuti ajambule nthano yao, kapena kumvetsera ku nthano ya sabatalo.

WEB

Aliyense angatengeko mbali mu nchitoyi pakulowa pa tsamba ya website nkupereka nthano pamenepo. Nthano zoperekedwazo, zizasandidwa nkukonzedwa ndipo zisasankhidwa ndi akatsiwiri kuti zitumizidwe ku onse otengako mbali. Nkothekanso upeza nkhokwe ya nthano zomwe zatumizidwa kale pa tsamba ya website iyi.

KHALANI AMODZI OTENGAKO MBALI MU LUSO IYI

Inunso mungathe kutengako mbali mu nchitoyi pofuna kupititsa patsogolo chikhalidwe chakuwerenga pakati pa ana achichepere mdziko ya Zambia. Zimene mufunika kuchita ndi kulemba zofunikila pa pepala ili m’munsimu ndi dzina lanu, zofunikila kuti tikufikeni ndiponso nthano yanu

Perekani tsopano

Submit your story

our partners

Contact Us

Get in Touch with Us

Creative Association International

Address: Plot 6831 Katimamulilo Road, Olympia Park
Lusaka, Zambia

Email: Angelam@crea-acr.com

Phone: +260-950-988-515